Anthu omwe anaphunzira pa seminale yaying’ono ya St. Paul the Apostle, mu dayosizi ya Mangochi ya mpingo wakatolika, awayamikira kamba kotengapo gawo popititsa patsogolo chitukuko cha dayosiziyi.
Episkopi wa dayosiziyi, Ambuye Montfort Stima, wanena izi loweruka pa mwambo wokondwerera nkhoswe ya seminaleyi yomwe ndi Paulo Woyera.
Iwo ati ndi udindo wa ophunzira omwe anaphunzira mu sukulu za mu dayosiziyi monga St. Paul kutukula sukulu komanso dayosiziyi.
“Ophunzira amene anaphunzira pa seminale imeneyi ena ndi ansembe komanso ena akugwira ntchito zosiyanasiyana tikuwakumbutsa kuti nthawi imene amachoka pa seminaleyi mpingo unali m’manja mwa azungu zimene zikutanthauza kuti chilichonse amachita ndi azungu. Koma lero tsopano mpingowu uli mmanja mwathu ifeyo eniake achikuda. Choncho tikuwapempha kuti ngakhale akukhala kutali ndi seminaleyi komanso dayosiziyi tikuwapempha kuti ndi luso lawo losiyanasiyana lomwe ali nalo athe kuthandiza mpingowu mu dayosiziyi,” anatero Ambuye Stima.
Iwo anati, “Tikudziwa kuti ena amadandaula nkhani ya ndalama koma kuthandiza sikulira ndalama zokha ayi koma ngakhalenso luso lomwe ali nalo atha kuthandiza dayosiziyi.”
Polankhulapo wapampando wa gulu la anthu omwe anaphunzira pa seminale-yi, a Montfort Howahowa, ayamikira mgwirizano omwe ulipo pakati pa ophunzira akalewa omwe wathandiza kutukula ntchito za bungweli komanso mwa zina kutukula sukuluyi ngakhalenso dayosiziyi.
“Titamva kuti dayosizi yakonza mwambowu, tonse omwe tinaphunzira pa sukuluyi, tinalumikizana ndi kusonkha pang’onopang’ono mpaka zinakwana zoti tayendetsera mwambo onsewu,” anatero a Howahowa.
Iwo ati ndi okonzeka kuthandiza dayosizi ya Mangochi ngati njira yoyankhirapo pempho lomwe episkopi wa dayosiziyi wapereka pozindikira kuti dayosiziyi ili pa mavuto aakulu komanso ngati njira imodzi yobwezera ulemu womwe dayosiziyi inawapatsa pa nthawi imene anali pa sukuluyi.