Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko wati chilango chakupha ndi chosayenera kamba koti munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi moyo.
Papa amalankhula izi potsatira msonkhano waukulu wa padziko lonse wa chisanu ndi chimodzi omwe uli mkati wofuna kuthetsa chilango chakupha omwe ukuchitikira mdziko la Norway.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, Papa Fransisko wati ndi ntchimo lalikulu kupereka chilango chakupha kwa munthu ngakhale atakhala kuti wapalamula mlandu waukulu.
Papa wapempha nthumwi ku msonkhanowu kuti zikambiranenso za chisamaliro chabwino m’ndende zosiyanasiyana za pa dziko lonse.