Nyumba zotsindikiza ndi kuwulutsa nkhani mdziko muno azilimbikitsa kuti zizifufuza mokwanira komanso kulemba mwaukadaulo nkhani zokhudza anthu olumala.
Wachiwiri kwa mkulu wa nthambi yophunzitsa zamalamulo pasukulu ya ukachenjede ya Chancellor, a Teleza Chome anena izi pambuyo pa pamaphunziro a tsiku limodzi a atolankhani okhudza maufulu a anthu olumala omwe anachitikira m’boma la Zomba.
Iwo ati atolankhani akuyenera kutengapo gawo popereka uthenga kwa a Malawi pofuna kuonetsetsa kuti maufulu a anthu olumala akulemekezedwa komanso kutetezedwa.
Maphunzirowa anachitika pansi pa mutu oti “Maufulu a anthu olumala: Uthenga ofunika kwa anthu onse” ndipo anachitika ndithandizo landalama lochokera ku bungwe la OSISA.
M’mau ake, mmodzi mwa amene amaphunzitsa atolankhaniwa, Dr Elizabeth Kamchedzera, anati atolankhani akuyenera kusankha bwino mau otchulira anthu amene ali ndi ulumale osiyanasiyana popewa kunyazitsa ndikupereka chithunzi cholakwika cha anthu oterewa.
M’modzi mwa amene amachititsa nawo maphunzirowa yamwenso ndi magistrate ku bwalo la milandu la Zomba, a Rhodrick Michongwe anatsindika kunena kuti nkhondo yolimbana ndikuteteza ufulu wa anthu olumala singayende bwino popanda kugwira ntchito limodzi ndi atolankhani.