Mpingo wa katolika mdziko muno wati ukugwirizana ndi ganizo la boma loti pasakhale lamulo lakupha munthu wopezeka olakwa pa mlandu wosowetsa komanso kupha anthu a mtundu wa chialubino.
Mlembi wa mkulu ku bungwe la ma episkopi mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM), bambo Henry Saindi anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.
Bambo Saindi ati mpingo wa katolika umalemekeza ufulu wokhala ndi moyo wa munthu aliyense ndipo suvomereza kuti munthu aphedwe ngakhale atapezeka wolakwa.
“Posachedwapa Papa Fransisko watsindikanso za ufulu ndi ulemelero wa moyo wa munthu kuti palibe amene ali ndi ufulu wochotsa moyo wa munthu wina ngakhale atakhala kuti munthuyo wapha mzake,” anatero bambo Saindi.
Iwo anati, “Mpingo ukugwirizana ndi ganizo la boma loti nkosayenera ndipo nkosaloredwa kuti boma lizipereka lamulo lonyonga kwa anthu amene apezeka ndi mlandu wopha kapena kuzembetsa ma ulubino.”
Bambo Saindi apempha anthu mdziko muno kuti akaneneze ku polisi munthu amene wapezeka akuchita mchitidwewu osati kupha komanso apempha mabwalo a milandu kuti azipereka chigamulo choyenera kwa anthu opalamula mulandu wotere.