Bungwe loteteza miyoyo ya anthu la mpingo wa katolika la PRO-LIFE lati kupha anthu a mtundu wa chialubino ndi kutsutsana ndi cholinga cha Mulungu kaamba koti iye analenga munthu aliyense m’chifaniziro chake.
Mkulu woyendetsa ntchito za bungweli, bambo Alpheus Dzikomankhani, anena izi pofotokozera Radio Maria Malawi pomwe imafuna kudziwa dongosolo lomwe bungweli lakhazikitsa pofuna kuteteza miyoyo ya anthu a mtunduwu.
“Kuphedwa kwa alubino ndi chimodzimodzi ndi kuphedwa kwa munthu wina aliyense chifukwa alubino ndi munthu wolengedwa ndi Mulungu monga alili munthu wina aliyense choncho kuphedwa kwa munthu aliyense ndi tchimo lalikulu pa maso pa Mulungu ndipo ndizosayenera,” anatero bambo Dzikomankhani.
Bambo Dzikomankhani apempha anthu mdziko muno kuti apemphere kolimba kuti agonjetse mchitidwewu.
“Pano tikudziwitsa anthu za kusamala moyo wa munthu kufikira pamene wamwalira. Pamene tikuchita zosayenera monga kupha alubino ndiye kuti moyo wa Mulungu wachoka mwa ife siifenso chifaniziro cha Mulungu ndipo ndiye kuti moyo wathu ndi chimodzimodzi ndi wa nyama,” anatero bambo Dzikomankhani.
Pamenepa Iwo apempha ma bwalo oweruza milandu kuti apitilize kupereka zilango zokhwima kwa munthu aliyense opezeka ndi olakwa pa mlanduwu.