Mpingo wa Anglican mdziko muno wati wayamba ntchito yophunzizitsa ndi kudziwitsa anthu za kuyipa kwa mchitidwe wopha ndi kuzembetsa anthu a mtundu wa chi alubino womwe padakali pano wakula mdziko muno.
Episkopi wa mpingowu wa dayosizi ya Upper Shire, Ambuye Brighton Vita Malasa anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pomwe imafuna kudziwa zomwe mpingowu ukuchita pofuna kuteteza miyoyo ya anthu amtunduwu.
Ambuye Malasa ati anthu a mtunduwu sakuyenera kusalidwa koma akuyenera kuwonetseredwa chikondi pofuna kusonyeza kuti iwo si osiyana ndi wina aliyense.
“Tayamba posachedwapa ma awareness, kuwadziwitsa anthu za zakuyipa kwa mchitidwewu. Ndikuwona kuti chimene chikusowa ndi chikondi. Zikanakhala bwino tikanamakondana wina ndi nzake. Ma alubino ndi anthu ngati ife tomwe, analengedwa mchifaniziro chake (Mulungu). Titati tibwerezeretse chikondi dziko lathu liyenda bwino. Ndipemphe boma, apolisi komanso aliyense wa ife kuti atengepo mbali pothetsa mchitidwe umenewu. Anthu asachite kukhala akapolo mdziko lawo lomwe kumalephera kugwira ntchito zawo,” anatero Bishop Malasa.
Ambuye Malasa apempha mabwalo amilandu kuti azipereka chilango choyenera kwa anthu opezeka ndi mlandu wopha komanso kuzembetsa anthu a mtunduwu, koma ati pasakhale lamulo lonyonga.
“Baibulo limaletsa munthu wina aliyense kupha mzake ndipo mpingo umalalika za chikondi. Ngakhale anthu atalakwa ndi anthube basi ndipo zisafike poti diso kulipa diso chifukwa izi zizatipanga tonse kukhala osawona. Ndiye ngati anthu apezeka olakwa titsatire malamulo chifukwa makhothi ndi amene apatsidwa mphamvu zoweruza. Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu choncho Mulungu yemweyo ndi amene ali ndi mphamvu yochotsa moyo wa munthu. Akalakwa alangidwe koma chilango choyenelera ndisanene ine chifukwa m’malamulo a dziko lino chinalembedwa,” anatero Ambuye Malasa.