Zigawenga za Boko Haram zapha anthu pafupifupi zana limodzi ndi makumi asanu sabata ino mchigawo cha Borno mdziko la Nigeria.
Anthu omwe awona izi zikuchitika awuza wailesi ya BBC kuti anthu a mfuti analowa mmudzi wina omwe uli pafupi ndi nyanja ya Chad lachitatu ndikupha anthu 97 kuphatikizapo amayi ndi ana.
Anthu ena 48 aphedwa lachiwiri atangomaliza mwambo wamapemphero omwe anali nawo mmidzi ina iwiri mdera lomwelo koma pa chiwembuchi amayi anasiyidwa.
Anthu ena afa paziwembu zosiyanasiyana zomwe zakhala zikuchitika mdzikolo musabata ino kufikitsa chiwerengero cha anthu omwe aphedwa musabata yokhayi pa 150.
Padakali pano malipoti a bungwe lomenyera ufulu wa anthu padziko lonse la Amnesty International akusonyeza kuti anthu 17 sauzande ndi omwe aphedwa ndi zigawengazi kuyambira mchaka cha 2009 pomwe zidayamba mtopola mdzikolo pofuna kukhazikitsa boma laulamuliro wa chisilamu