A ku likulu la chipani cha Rosarian Sisters mu dayosizi ya Mzuzu alengeza za imfa ya Sister Maria Rita Moyo.
Sister Moyo anabadwa mu chaka cha 1948 ndipo anachita malumbiro awo oyamba mu chipanichi pa 28 August mu chaka cha 1969.
Pa nthawi ya moyo wao Sister Moyo anagwirapo ntchito ngati mphunzitsi wa ku pulayimale komanso amakonda kuyimba nyimbo za ambuye yesu okhala mu sacrament la Ukaristia.
Thupi la malemu Sister Moyo aliyika lachiwiri pa 28 June 2016.
Mzimu wa Sister Maria Rita Moyo uuse mu mtendere wosatha.