Bwalo la milandu la Midima ku Limbe mu mzinda wa Blantyre lalamula anthu khumi ndi awiri 12 kuti apereke chindaputsa cha ndalama zokwana 5 sauzande aliyense kaamba kopezeka akuchita malonda pa malo oletsedwa mtawuni ya Limbe mu mzinda wa Blantyre.
Wapolisi wotengera milandu ku polisi ya Limbe Sergent Steve Mpira anauza bwaloli kuti anthuwa anawagwira m’misewu ya tawuni ya Limbe lachiwiri.
Sergent Mpira ati apolisi mogwirizana ndi anthu ena ogwira ntchito ku khonsolo ya mzindawu anali pa ntchito yofuna kuchepesa mchitidwe ogulitsa malonda m’malo olakwika.
Pamenepa Sergent Mpira anapempha oweruza milandu ku bwaloli kuti apereke chilango chokhwima kwa anthuwa potengera kuti milandu ya mtunduwu ikuchuluka mu mzinda wa Blantyre.
Popereka chigamulo, oweruza milandu ku bwaloli, a Benedictus Chitsakamire anati anthu omwe amagulitsa malonda m’malo olakwika amakolezera milandu ing’ono ing’ono monga yopisa anthu m’matumba kamba koti mbava zimatengerapo mwayi kamba ka mpungwe-pungwe omwe a malondawa amadzetsa m’misewu.
Pamenepa a Chitsakamire anati anthuwa sapereka msonkho zomwe zimabwezera m’mbuyo chitukuko cha mmakhonsolo.
Katundu yemwe anawapeza anthuwa akugulitsa ndi monga zipatso za apozi, masefa a ufa, zakumwa zoziziritsa kukhosi ndi zina zambiri.