Maepiskopi a mpingo wakatolika mdziko la South Africa adzudzula mchitidwe wa ziwawa omwe ukuchitika mdzikolo potsatira chisankho cha makhansala chomwe chikuyembekezeka kuchitika mwezi wa mawa.
Malinga ndi uthenga omwe bungwe la maepiskopi latulutsa omwe wasainidwa ndi wapampando wa chilungamo ndi mtendere mu bungweli, Ambuye Abel Gabuza wapempha mamembala onse a zipani za ndale kuti akakhale nawo pa mwambo wa mapemphero opemphelera mtendere omwe uchitike lachitatu sabata la mawa.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, Ambuye Gabuza ati mtendere mdziko la South Africa sukuyenera kutengedwa ngati chinthu chapafupi ndipo mzika ngakhalenso zipani za ndale za mdzikolo zikuyenera kukhala ndi udindo wodzetsa mtendere makamaka pa nthawi ya chisankho.
Ambuye Gabuza adzudzulanso zipani za ndale zomwe zimagwiritsa ntchito achinyamata kuchita ziwawa ndipo apempha achinyamatawa kuti asalole kugwiritsidwa ntchito ndi zipanizi.
Pomaliza kalatayi yapempha mzika zoyenelera za dzikoli kuti zikaponye nawo voti pa chisankhochi ndi kukasankha atsogoleri oti awayimilire moyenera.