Akhristu a mpingo wakatolika m`dziko muno awapempha adzitenga gawo lalikulu pothandiza Radio Maria Malawi.
Yemwe anali mlendo wolemekezeka pa mwambo wotsekera ntchito yotolera thandizo la wailesiyi lotchedwa Mariatona, Wolemekezeka a Mark Katsonga Phiri anena izi ku Michiru Shrine mu arkidayosizi ya Blantyre.
Iwo ati Radio Maria Malawi pomwe ikugwira ntchito yofalitsa uthenga wa Mulungu, ikukumananso ndi mavuto a nkhaninkhani zomwe ati zikufunika kuti akhristu onse a mpingowu azichita msonkhansonkha ngati umenewu.
Pa mwambowu, Radio Maria Malawi yapereka certificate kwa m’modzi mwa abwenzi a wailesiyi mayi Veronica Sembereka kaamba kotolera ndalama zambiri pa mariatona wa chaka chinoyu.
Ndipo m’mawu ake Director wa Radio Maria Malawi bambo JosephKimu ati zomwe akhristu achita chaka chino ndi chitsimikizo choti anthu ambiri amayikonda wailesiyi.
Yemwe anali wolemekezeka pa mwambowu a Mark Katsonga Phiri apereka ndalama yokwana 1 million Kwacha ndipo chaka chino Radio Maria Malawi yakwanitsa kupeza mulingo wa ndalama zomwe inayerekeza kuti ipeze wa 10 million kwacha.