Amuna awiri ali m’manja mwa apolisi atapezeka akubera mayeso a fomu 4 m’boma la Balaka.
M’modzi mwa amunawa a Joseph Makiyi omwe amagwira ntchito ku Prison Fellowship anatenga tchuthi kuntchito kwawo kuti akukalemba mayeso a MSCE ku Balaka Islamic Institute ndipo m’malo mwake anapempha mzawo a Charles Kumwenda omwe amagwira ntchito ngati wa zaumoyo pa chipatala cha Kapire m’bomalo kuti akawalembere mayesowo.
Masana a tsiku la pa 30 June pamene ophunzira amalemba mayeso a Human Geography ndi pamene mkuluyi anagwidwa ndi m’modzi mwa ogwira ntchito ku MANEB yemwe anafika kudzayang’nira m’mene mayeso amayendera pa malopa.
Pakadali pano amuna awiriwa avomera mlanduwu ndipo akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu ndikukayankha mulandu wobera mayeso.
Amunawa amachokera m’mudzi mwa Lupanga mfumu yaikulu Nsamala m’boma la Balaka.