Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Akhristu Awayamikira Kamba Kopulumutsa Montfort Press

$
0
0

Akhristu a mpingo wakatolika mu Arkdayosizi ya Blantyre awayamikira kamba ka mgwirizano omwe wathandiza kupulumutsa malo a mpingowu a Montfort Press.

Arkepiskopi wa Arkdayosiziyi Ambuye Thomas Luke Msusa alankhula izi ku parishi ya St. Peter and Paul ku Chilobwe pa mwambo wopereka sakramenti la Ulimbitso ku parishiyi.

Iwo ati ndi okondwa kuti akhristu a mpingowu mu arkidayosiziyi anadzipereka ndi chuma chawo zomwe zathandiza kupulumutsa malo a Montfort Press omwe padakali pano pali sukulu ya sekondale ya James Chiona.

“Nditafika kumene kuno ku Blantyre ndipo nditayamba kuwona ndinawona zabwino zambiri komanso katundu wolemetsa. Katundu woyamba yemwe akhristu munandithandiza kusenza ndiye Montfort Press. Zinali zovuta koma nditangoyankhula mkhristu aliyense anatipatsa mphatso zosiyanasiyana moti lero pano kulibe Montfort Press koma kuli James Chiona High School.

Tikunena pano momwe munali Montfort Press muja akuphunziramo ndi anyamata athu moti pa 18 July pano ofuna kukayamba kumeneku fomu 1 mpaka 3 achita ma interview awo. Zonsezi ndi chifukwa cha kudzipereka kwa akhristu a kuno ku Blantyre arkidayosizi,” anatero Ambuye Msusa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>