Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mtukula Pakhomo Wapindulira Mabanja Ambiri ku Mulanje

$
0
0

Bungwe la OXFAM mdziko muno lati ndalama za ntchito ya mtukula pakhomo zapindulira anthu anthu ambiri m’boma la Mulanje.

Mkulu wa bungweli mdziko muno a John Makina alankhula izi ndi Radio Maria pomwe amafuna kudziwa momwe ndalamazi zagwilira ntchito.

Iwo ati anthu ambiri omwe analandira nawo ndalamazi azigwiritsa ntchito moyenera potengera ndi mavuto omwe ali nawo.

“Anthu anali ndi mwayi wolandira ndalama  zimene amatha kugwiritsa ntchito pogula zosoweka pakhomo monga chakudya, school fees kugula feteleza ndi zina zambiri. Ndalama zimenezi ena akumazisungitsa ku banki mkhonde ndi cholinga choti zizawathandize patsogolo chifukwa timawaphunzitsa kuti asamangodalira zomwe alandira koma aziwonanso za kutsogolo. Tikulimbikitsanso anthu kuti athe kugwiritsa ntchito mbaula zomwe zingathe kuteteza chilengedwe,” anatero a Makina.

A Makina ati bungwe lawo lipitiriza ndondomekoyi komanso njira zina zomwe zingatukule makomo. Iwo ati alumikizananso ndi mabungwe ena ndi cholinga chotetsa njala mdziko muno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>