Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dayosizi ya Chikwawa Ipempha Thandizo la Chakudya

$
0
0

Dayosizi ya mpingo wa katolika Chikwawayapempha anthu komanso mabungweakufuna kwabwino kuti athandize anthu okhala m’dera la kunsi kwa m’tsinje wa Shire omwe akhudzidwa kwambiri ndi mavuto a njala.

Episikopi wa dayosizi-yi, olemekezeka ambuye PeterMusikuwa anena izi pa mwambo wokhadzikitsa ntchito yogawa chakudya kwa anthu omwe akhuzidwa ndi mavuto-wa mu dayosizi-yo.

Iwo ati dayosizi yawo ya Chikwawa yakhadzikitsa ntchitoyi pofuna kuthandiza anthu okhudzidwa-wa ndi chakudya.

“Takhazikitsa ntchito imeneyi ngati njira imodzi yofuna kuthandiza anzathu amene ali ndi vuto la chakudya. Vutoli labwera chifukwa cha madzi osefukira amene anachitika kuno ku dayosizi ya Chikwawa pamene anthu ambiri anawononga miyoyo yawo komanso katundu wambiri anawonongeka. Chaka chinonso kwabwera ng’amba, anthu ambiri akusowa chakudya. Choncho tinawona kuti tiwathandize anzathu amenewa ndiye tinapempha anzathu aku Germany  ndipo antithandiza ndi ndalama zomwe takwanitsira kutsegulira program imeneyi,” anatero a Musikuwa.

Iwo ati program yi ifikira anthu onse amene ali ovutikitsitsa mu dayosizi yonse ya Chikwawa. Iwo anatsindika kuti sikuti izi zingathetse njala koma ati zitangochepetsa chabe.

 Mfumu masisi ya mderali inathokoza mpingowu kamba kobwera poyera ndikuthandiza anthu amene akuvutika ndi njala pakadali pano.

Pali chikonzero choti dayosiziyi igawa matumba 105 ku parishi iliyonse mu dayosiziyi omwe ndi maboma a nsanje, chikwawa ndinso mbali ina ya Thyolo. Chithandizo chogulira chakudyachi chachokera kwa abwenzi a dayosiziyi a mdziko la Germany.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>