Kuwomberana kwa mphamvu kwabuka mu mzinda wa JUBA mdziko la South Sudan pakati pa asilikali aboma ndi asilikali a yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikolo.
Kuwomberanaku komwe kunayamba lachisanu pakati pa anthu otsatira mtsogoleri wa dzikolo a SALVA KIIR ndi yemwe anali wachiwiri wawo a REIK MACHAR kwaphetsa anthu oposa zana limodzi 100.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, kumenyanaku kunabuka pomwe anthu awiriwa amachita zokambirana ku nyumba ya boma ya dzikolo.
Kusamvana pakati pa magulu awiriwa kunayamba mu chaka cha 2013 pomwe Pulezident KIIR anachotsa pa udindo wachiwiri wakeyu a Marchar ati powaganizira kuti amafuna kulanda boma.