Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kwaya One ya Mtsilo Yapindula ndi Radio Maria Malawi

$
0
0

Kwaya One ya Mtsilo ku parish ya Mponela mu arkidayosizi yaLilongwe ya mpingo wakatolika yati yapindula pa ulendo wake woyendera wailesi ya Maria ku Mangochi.

Wapampando wa kwayayi a Rabson Joseph anena izi polankhula ndi Mtolankhani wathu yemwe amafuna kudziwa momwe kwayayi yapindulira pa ulendo wake wa masiku atatu womwe akhala ali kulikulu la wailesiyi.

Iwo ati akwaniritsa zolinga zawo monga kujambulitsa ma pologalamu komanso kuthandiza achinyamata amene amatumikira ku wailesiyi.

“Tapindula kwambiri kuno ku Radio Maria Malawi komanso ngati kwaya zatipatsa chilimbikitso ndipo tawona kuti tili ndi kuthekera kochita zinthu zina zomwe sitimaziganizira. Taphunzira komanso takwaniritsa maso mphenya athu azathandiza achinyamata amene amatumikira kuno ku Radio Maria Malawi ndi kangachepe; chimanga matumba atatu ndi ti ndalama,” anatero a Joseph.

Pamenepa a Joseph apempha anthu onse mdziko muno kuti azithandiza Radio Maria Malawi ndi kangachepe komwe ali nako.

“Kunoku kulibe mulingo weniweni wothandizira. Ndi kangachepe kalikonse komwe tili nako tith kuthandiza wailesiyi. Aliyense atengepo gawo makamaka ife akhristu chifukwa wailesiyi imafikira kwambiri ife akhristu. Tisamangoyimva wailesiyi kuma tichitepo kanthu poyithandiza,” anatero a Joseph.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>