Amayi a mpingo wakatolika mu dayosizi ya Zomba ati amadziwa zakufunika kothandiza asemino omwe akuchita maphunziro awo pa seminale yaying’ono ya Nankhundamudayosizi-yi.
Wapampando wa bungwe-li mu dayosizi-yi mayi Elizabeth Meke anena izi pomwe amayi-wa amakapereka thandizo la katundu wosiyanasiyana pa seminale-yi.
Iwo ati aganiza zokapeleka thandizolo pofuna kuonetsa umodzi wawo pa ntchito zothandiza seminale-yi.
“Tili ndi udindo waukulu monga kubwera kuno kuzawona asemino athu ndi cholinga choti kutsogolo kuno azakhale ansembe athu otitumikira ife tomwe. Ansembe ndi ochepa ndi timanena kuti munda ndi waukulu koma antchito ndioperewera,” anatero mayi Meke.
Poyankhula m’malo mwa bambo mfumu a seminaleyi bambo Micheal Chipoya ati thandizoli lafika munthawi yake pamene achinyamata pa seminaleyi akusowa chithandizo.
“Ndife okondwa chifukwa cha chikondi chomwe amayiwa amatiwonetsa potiyendera chaka ndi chaka kuzatipatsa mphatso zosiyanasiyana zothandizira seminale yathu. Maseminale ambiri mdziko muno akuvutikabe kuti akhale odziyimira pawokha koma ndi thandizoli ndiye kuti tiyenda bwinobwino mosavutika mpaka chaka timaliza. Ndi chifundo cha Mulungu kuti watikonda kwambiri komanso tikudziwa amayi athuwa amatikonda kwambiri,” anatero bambo Chipoya.
Zina mwa zinthu zomwe zaperekedwa pa tsikuli ndi monga sopo, mchere, bread, sugar, matumba 20 a chimanga, mbatata, mtedza ndi zina zambiri.