Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

UN Yapempha Bata Mdziko la South Sudan

$
0
0

Nthambi yowona za chitetezo ku bungwe la United Nations (UN)lapempha magulu awiri omwe akumenyana mdziko la South Sudan kuti athetse kusamvana komwe kulipo pakati pawo pofuna kupewa zamtopola kuti zingafalikire m’madera ena.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC uthenga omwe nthambiyi yatulutsa wati nthambiyi ndi yokhudzidwa ndi mchitidwewu pozindikiranso kuti magulu awiriwa amachitira zamtopolazi pa nyumba ya bungwe la UN mdzikolo.

Padakali pano nthambiyi ati yatumiza asilikali oti akathandize kudzetsa mtendere mdzikolo.

Malipoti ati anthu pafupifupi mazana awiri afa potsatira kumenyana kwa pakati pa asilikali a mtsogoleri wa dzikolo a Salvar Kiir ndi asilikali a yemwe anali wachiwiri wake a Riek Marchar komwe kunayamba lachisanu sabata yatha.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>