Dayosizi ya Zomba ya mpingo wakatolika yapempha akhristu ogwira ntchito muzipatala kuti akhale olimba pa chikhristu chao komanso akuyenera kuzindikira kuti mpingo umawaganizira.
Episkopi wa dayosiziyi Ambuye George Desmond Tambala alankhula izi lamulungu pomwe amakachezera anthu ogwira ntchito ku chipatala chachikulu cha Zomba.
Iwo awuza anthu ogwira ntchito ku chipatalawa kuti asabwelere m’mbuyo pa chikhristu chawo kamba koti mpingo umazindikira ntchito yabwino yomwe amagwira.
“Chigawo chachikulu cha ntchito ya ambuye yesu amathandiza odwala. Ine ndabwera pano kuti tipitirize ntchito imeneyi. Ndimadzawalimbitsa kuti akhale olimba pa chikhulupiliro chawo komanso kuti mpingo ukukhuzidwa kwambiri ndi ntchito yawo komanso umadziwa zimene anthuwa amakumana nazo. Ndiye ngati mpingo tikufuna tiwathandize tiwalimbikitse pa ntchito yabwino imene amagwira,” anatero ambuye Tambala.
Ambuye Tambala ati akulimbikitsa kugwira ntchito mwadongosolo (strategic plan) yomwe ati ifikiranso ku chipatalachi.