Anthu asanu ndi atatu (8) afa ndi moto umene unabuka pa malo ena opelekerapo chisamaliro cha ana amasiye ndi ovutika a Key of Hopeku Durban m’dziko la South Africa.
Malingana ndi malipoti a wailesi ya BBC, mwa anthu omwe afawo pali ana asanu ndi m’modzi (6).
Malingana ndi malipoti, motowo unabuka kuyambira mbali ina yomwe kumakhala anawa. Padakalipano aku nthambi yopulumutsa anthu pa ngozi m’dzikomo mogwilizana ndi a polisi akhadzikitsa ntchito yofufuza bwino gwero la ngoziyi.