Ofesi ya za maphunziro mu zoni ya Chimwala yayamikira sukulu ya m’mera mpoyamba ya St. John yomwe ili m’dera la a Senior Chief, Chimwala m’boma la Mangochikamba kodzipeleka pa ntchito zotukula maphunziro a ana m’bomalo.
A Cliff Mjojo, omwe anayimira mkulu wa ku ofesi-yi ndi omwe anena izi pa mwambo wopereka ma certificate kwa ana amene amaliza maphunziro awo a m’mera mpoyamba pa sukulu-yi.
A Mjojo ati sukuluyi ikuthandiza kwambiri potukula maphunziro mderali.
“Ana amene amachokera pa St. Johns Nursery School samativutitsa akabwera ku paulaimale. Amachititsa ntchito yathu kukhala yophweka kamba koti amakhala atawatsegula kale m’mutu,” anatero a Mjojo.
Senior Chief Chimwala yemwe sukuluyi ikupezeka mdera lake wayamikira bambo Joseph Kimu kamba ka chidwi chomwe akuwonetsa pa ntchito za maphunziro mdera lake.
“Ine ndimathokoza bambo Joseph Kimu pa zomwe akutichitira kuno ku dera langa makamaka potsegula sukulu zmenezi zammera mpoyamba. Mwana amayenera ayambe maphunziro ake adakali wachichepere ndipo amazachita bwino,” anatero Senior Chief Chimwala.
Mayi Anusiata Kanyika omwe anayimira mkulu wa sukuluyi omwe ndi bambo Joseph Kimu anati akufunitsitsa kuti dera la Senior Chief Chimwala lizakhale ndi anthu ophunzira bwino omwe azathe kutukula derali komanso dziko la Malawi.
“Tikufuna muzachoke president mdera lino, ma nurse, madotolo, aphunzitsi, ansembe ndi ena ambiri. Ana tikawayamba chonchi sitimangowasiyira pa nursery ayi timawayang’anirabe ku pulaimale, sekondale mpaka ku koleji ndi cholinga choti adzakhale oyima pawokha komanso azatukule dziko lino tsiku lina ataphunzira bwino,” anatero mayi Kanyika.
Mkulu woona zachuma pa sukuluyi mayi Agness Odala wati makolo ambiri ali ndi ana omwe akungokhala osawapititsa ku sukulu kamba ka mwina zipembezo, zilankhulo komanso zikhulupiliro zosiyanasiyana.
“Ambiri ali ndi ana m’makomomu koma safuna kuwabweretsa kuti tiwaphunzitse. Ena amati mwina kuno azadya nkhumba monga mudziwa dera lino ndi la anthu ambiri achisilamu. Ndiye ine ndikuwapempha makolowa kuti ayambe kuwona za tsogolo la ana awo,” anatero mayi Odala.
Patsikuli ana amene alandira ma certificate kuwavomereza kuti akayambe standard 1 msukulu zosiyanasiyana alipo 157.