Bungwe lolemba ndi kupereka ziphaso za m’dzika za dziko lino la National Registration Bureau (NRB) lati layamba ntchito yolemba komanso kupereka ziphaso-zi.
M’neneri wa bungweli a Norman Fulatira ndi yemwe wanena izi polankhula ndi Mtolankhani wathu amene amafuna kudziwa momwe ntchito-yi yayambira . A Fulatira ati pakadali pano ntchito-yi yayamba bwino.
“Tayamba ndi akuluakulu a m’boma amene tawajambula monga ma PS, ma director ndi ena. Tinapezeraponso mwayi pamene aphungu akukumana ku nyumba ya malamulo moti tawajambula onse. Tikachoka apo tiyamba ntchitoyi mmaboma khumi ndi limodzi (11) omwe tawasankha momwe tasankhamonso mwina mudzi umodzi pena iwiri,” anatero a Fulatira.
Iwo ati pakadali pano akufuna kulemba anthu 6 thousand ndipo chaka chomwechino ayambanso gawo lachiwiri momwe alemba anthu okwana 90 thousand ndipo gawo la ntchitoyi lachitatu lomwenso ndi lotsiriza lizayamba kumayambiliro kwa chaka cha mawa lomwe azalembe anthu onse mdziko muno.
A fulatira ati ntchitoyi akuyigwira ndi ndalama zomwe boma la dziko la Malawi lapereka.
“Boma chaka chatha anatipatsa ndalama zokwana 1.5 billion kwacha zogulira zipangizo komanso zoyambira ntchito imeneyi mgawo loyamba. Zipangizo zabwera ndipo takonzeka kugwira ntchito imeneyi. Pa budget ya chaka chino bomanso latipatsa ndalama zina zomwe tigwilire ntchito gawo lachiwiri. Koma gawo la chitatu boma lizalumikizana ndi maiko akunja amene amatithandiza kuti aztithandize pa ntchitoyi,” anatero a Fulatira.