Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all 1875 articles
Browse latest View live

Khansa ya Khomo la Chiberekero, Chiwopsezo Cha Miyoyo ya Amayi

$
0
0

Nthenda ya khansa ya mchiberekero akuti ndi imodzi mwa matenda omwe akupitilira kutenga miyoyo ya amayi kamba koti amayi ambiri samapita kukayezetsa kuti adziwe ngati ali ndi matendawa kapena ayi.

Mmodzi mwa akatswiri ophunzitsa anamwino mdziko muno Professor Address Malata, yemwenso ndi mkulu wa sukulu ya anamwino ya Kamuzu College of Nursing KCN,ndi yemwe wanena izi polankhula ndi mtolankhani wathu mu mzinda wa Blantyre pambuyo pa sabata imodzi yoganizira matendawa yomwe inachitika posachedwapa.

Professor Malata awuza Radio Maria Malawi kuti nthendayi ndi yochizika koma imafunika idzwike msanga isadafike poyipa.

Iwo ati amayi ambiri amamwalira ndi matendawa kamba kosowa ndalama zopitira kunja kukalandira thandizo la matendawa kamba koti pamafunika ndalama zochuluka.

“Amayi ambiri amene amamwalira mdziko muno amamwalira ndi khansa ya khomo la chiberekero zomwe dziko la Malawi likufunika kutengapo gawo poteteza amayiwa,” anatero a Malata.

Pamenepa mayi Malata apempha atsikana kuti asamayambe kugona ndi amuna ali achichepere kamba koti ali pa chiopsezo chopezeka ndi matendawa.

Masiku apitawa chipatala cha Mwayiwathu chinali pa dongosolo loyesa amayi ngati ali ndi matendawa mwa ulere.

Polankhula mmodzi mwa madotolo pa chipatalapo Dr Bonus Makanani ati izi zathandiza amayi ambiri kudziwa mmene alili,ndipo amene apezeka ndi nthendayi awauza chochita.

Dr Makanani ati, “amayi amene apezeka ndi matendawa ali ndi mwayi wolandira thandizo ngati angakwanitse, koma enawo tawatumiza ku chipatala chachikulu cha QUECH kuti akalandire thandizo.”

Matenda a khansa ya khomo la chiberekero akupezeka ndi amayi a mmayiko amene akukwera kamba koti amayi sakhala ndi chidwi chokayezetsa matendawa.

 


Mzimayi Afa ndi Nthaka Yogumuka

$
0
0

Mayi wa zaka 62 wamwalira ndipo ena awiri awagoneka pachipatala cha Dowa atavulala kwambiri nthaka itawagumukira m’boma la Dowa.

Mneneri wa   apolisi m’bomalo Sergent Richard Kaponda watsimikiza za nkhaniyi. Sergent Kaponda wati ngoziyi, yachitika pomwe anthuwa amafukula dothi lomwe amafuna kukakongoletsera nyumba zawo pa mpikisano wa mupulojekiti ina yomwe opambana akuyembekezeka kudzalandira mphotho.

Kaponda wati amayiwa ali mkati mofukula dothilo nthaka inagumuka ndi kuwaphinja ndipo mayiyo wamwalira pa malo a ngozi omwewo.

Zotsatira zakuchipatala zasonyeza kuti mayiyo Namatochi Isaac wammudzi mwa Mwaza kwa mfumu yayikulu Chiwere m’bomalo wamwalira  kamba kovulala kwambiri mmutu.

Dziko la Zimbabwe lati Libweza Malo omwe Lidalanda kwa Azungu

$
0
0

Dziko la Zimbabwe lati libweza  malo omwe lidalanda azungu zaka khumi ndi zisanu zapitazo pofuna kubwezeretsa phindu lomwe dzikolo limapeza paulimi omwe azungu amachita mmalowo.

Malipoti a News24 ati nduna yowona za malo mdzikolo a Douglas Mombeshora yatsimikiza kuti boma la pulezidenti Robert Mugabe lidalanda malowo ndipo lalamula kale atsogoleri onse amzigawo kuti apereke mayina a azungu omwe atsogoleriwa akufuna kuti abwezeredwe malo omwe amkagwiritsa ntchito,maka okhawo omwe akupereka chiyembekezo kuti adzathandiza potukula chuma cha dzikolo.

Malipoti akusonyeza kuti chuma cha dzikolo chidapita pansi kwambiri,mwa zina azungu atalandidwa malowo ndikuwapereka kwa mzika za dzikolo zomwe zimalephera kuwagwiritsa bwino ntchito kamba kosowa zipangizo zomwe zingawathandize kulima minda ikuluikulu.

Pulezidenti Museveni Adzetsa Mtendere Mdziko la Burundi

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la Uganda Yoweri Museveni wayamba zokambirana zofuna  kudzetsa mtendere pakati pa boma ndi magulu otsutsa mdziko la Burundi pomwe magulu otsutsawo sakugwirizana ndi mfundo yoti Pulezidenti wadzikolo Pierre Nkuruzinza ayimenso kachitatu pa mpando wa upulezidenti.

Malipoti akusonyeza kuti pulezidenti Museveni lachiwiri sabata ino anakumana ndi nthumwi za boma komanso akuluakulu otsutsa boma mdzikolo.

Polankhula asanayambe mkumano ndi akuluakulu ambali ziwirizi pulezidenti Museveni anapempha atsogoleriwo kuti awonetsetse kuti pakhale umodzi pakati pawo.

Iye wati ndi wokondwa kuti boma la dzikolo lathetsa  gulu la achinyamata lomwe linakhazikitsa ndi cholinga choti lidzichitira anthu  zamtopola.

Pulezidenti Museveni yemwe wakhala akulamulira dziko la Uganda kuyambira mchaka cha 1986 anasankhidwa kukhala mkhala pakati pa zokambirana zapakati pa boma ndi akumbali yotsutsa, pakusamvana komwe kwabuka mdziko la Burundi-lo.

Chisankho cha pulezidenti mdzikolo chikuyembekezeka kuchitika lachiwiri pa 21 mwezi uno.

Papa Benedicto Abwelera ku Vatican

$
0
0

Mtsogoleri wopuma wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Benedicto wa 16 wabwelera ku likulu la mpingowu ku Vatican atakhala sabata ziwiri ku nyumba ya a Papa ya Castel Gandolfo mdziko la Italy.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya mpingowu ya Vatican,papa Benedikito opuma,wayamikira Meya wa mzinda omwe nyumbayo ili mdzikolo,kamba komulandira komanso kukhala bwino pa nthawi yomwe anali mderalo.

Papa Benedikito wachi 16 opuma anafika mderalo pa 30 mwezi watha,komwenso anapezerapo mwai ocheza kwa tsiku limodzi  ndi mtsogoleri wa mpingowu padziko lonse Papa Francisco.

Vuto la Madzi Lakula Mdera la Mchesi

$
0
0

Anthu okhala ku Mchesi m’boma la Lilongwe apempha boma kuti liyambe msanga kupereka madzi awukhondo pogwiritsa ntchito mipopi yomwe idamangidwa kale mderalo.

Malinga ndi m’modzi mwa anthu okhudzidwa mdelalo a Petias Kalichero anthu mderalo maka amayi akuvutika kwambiri kuti apeze madzi abwino, zomwenso zikukhudza kwambiri miyoyo yawo ya m’banja.

A Kalichero ati mderalo munamangidwa kale mipopi ya madzi, koma sidayambe kugwira ntchito, ndipo apempha boma kudzera ku bungwe lopereka madzi mumzinda wa Lilongwe la Lilongwe water board kuti lichitepo kanthu msanga mvula yambiri isanayambe kugwa pofuna kuti anthu mderalo adzimwa madzi awukhondo.

Iwo ati, “kuno ku Mchesi vuto la madzi ndi lalikulu kwambiri, tikuthokoza boma kuti linatimangira malo a madzi koma chomwe tikupempha ndi chakuti atithandize mwachangu kuti madzi ayambe kutuluka.”

Pamenepa a Kalichero anati ndi zomvetsa chisoni kuti amayi ambiri amadzuka usiku kukatunga madzi zomwe sizipereka ulemu ku mabanja ambiri mderali.

“Amayi akumadzuka 2 koloko ya usiku kupita kukasaka madzi zomwe chiwopsezo chake ndi chakuti mabanja amasokonekera kamba koti abambo si ambiri amene amakhulupilira kuti akazi awo apita ku madzi,”anatero a Kalichero

Pomwe Radio Maria Malawi imafuna kumva zambiri pa zomwe zikulepheretsa kuti mipope yomwe yadzalidwa mderalo iyambe kugwira ntchito,akuluakulu a ku Lilongwe water board samayankha lamya zawo.

Atsogoleri Mmadera Akhale Patsogolo Pokhwimitsa Chitetezo

$
0
0

Apolisi m’boma la Balaka apempha atsogoleri a mmagulu osiyanasiyana kuti atengepo gawo lalikulu pantchito yokhwimitsa chitetezo m’bomalo.

Mkulu owona ntchito za apolisi akumidzi mbomalo Sub-Ispector Roster Milanzindi yemwe wapempha maguluwa lachisanu pamsonkhano omwe anakonzera magulu osiyanasiyana akumidziomwe unachitikira kulikulu la mfumu yayikulu Chamthunya m’bomalo.

Milanzi wati pamene dziko lino likukumana ndi vuto la kuchepa kwa chitetezomagulu osiyanasiyana akuyenera kutengapo gawo lalikulu pofuna kubwezeretsa chitetezo pakati pa anthu pomwe vuto la kuchepa kwa chitetezo lakula kwambiri mdziko muno.

Iye wati pofuna kukwaniritsa ntchitoyianthu akuyenera kudziwa bwino za anthu omwe amakhala nawo pafupi, ndikukanena kupolisi akakayikira chilichonse mwa iwo.

Pothilirapo ndemanga mfumu yayikulu Chamthunya yalonjeza kuti ichita chotheka pokhwimitsa chitetezo mdera lake ndipo  yalimbikitsanso  amayi kuti asamabise anthu omwe aphwanya ufulu wawo komanso wa ana.

Papa Francisco wati Ntchito za Migodi Zikomere Anthu Okhala Moyandikana ndi Malowa

$
0
0

Mtsogoleri wampingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco,wapempha mayiko kuti adziwonetsetsa kuti ntchito za migodi zomwe zikuchitika mmayiko awo zikuchitika mokomera anthu  onse maka oyandikana ndi malo omwe migodiyo ikuchitikira.

Papa Francisco,wapereka pempholi muuthenga wake omwe atumizira nthumwi zomwe zili kumsonkhano okhudza chitukuko cha migodi ndi zotsatira zake,omwe ukuchitikira ku likulu la mpingowu ku Vatican.

Cholinga cha msonkhanowo omwe wakonzedwa ndi nthambi yowona za chilungamo ndi mtendere kulikulu lampingowu ndi chofuna kuwunika madandaulo omwe anthu okhala mmadera oyandikana ndi migodi amakumana nawo nthawi zonse.

Mmawu ake mkulu owona zamabungwe a mumpingowu kulikululo Kadino Peter Turkson, wati nthawi zambiri ntchito zamigodi zimabweretsa mavuto monga kuwonongeka kwa chilengedwe ndipo ndi pofunika kuti mayiko aziganizira mbali zonse akafuna kuyambitsa ntchitozi.


Atsogoleri a Zipani Zotsutsa Sapikisana Nawo pa Chisankho cha Pulezidenti Mdziko la Burundi

$
0
0

Pamene chisankho cha pulezidenti mdziko la Burundi chikuyembekezeka kuchitika lachiwiri, mtsogoleri wa dzikolo Pierre Nkurunziza ati akuyembekezeka kupambana pa chisankhochi zomwe zichititse kuti akhale pa ulamuliro wa dziko logawikana.

Malinga ndi malipoti a NEWS24 zipani zotsutsa ndi magulu omwe si aboma akana kutenga nawo mbali pachisankhocho ndipo ati zomwe achita a Nkurunziza ndi zotsutsana ndi malamulo komanso kuphwanya mgwirizano wa mtendere womwe unakhazikitsidwa mdzikolo mu chaka cha 2006 pambuyo pa nkhondo ya pachiweniweni yomwe inachitika mdzikolo.

Chisankhocho chomwe otsutsa akana kupikisana nawo ati kamba koti ndi chobera, Pulezidenti Nkuruzinza alibe wopikisana naye.

Mmodzi mwa akuluakulu otsutsa mdzikolo wati boma la dzikolo ladzipatula kuti lichite chisankhocho litakanika kumvana pa zokambirana zodzetsa mtendere zomwe amachititsa mtsogoleri wa dziko la Uganda a Yoweri Museveni.

Mutharika Wati Boma Lake Silatsankho

$
0
0

Mtsogoleri wadziko lino Professor Arthur Peter Mutharika  wati sizowona zomwe anthu ena akumanena zoti  boma lake limapanga tsankho posankha anthu m'maudindo.

Mutharika amayankhula izi lamulungu pamsonkhano omwe anachititsa pa sukulu yapulaimale ya Nyambadwe mumzinda wa Blantyre.

Iye wati boma lake likuyesetsa kumayika anthu mmaudindo poyang’anira zoyenereza zomwe ali nazo.

Pamenepa pulezidenti Mutharika anapereka zitsanzo za akuluakulu monga mkulu wazamalamulo yemwe amachokera mchigawo chakumpoto, mkulu wa asilikali yemwe ndi wamdera lakumvuma ndinso ena ambiri.

Mwazina pamsonkhanowu Pulezidenti Mutharika analongosolanso zina mwa zitukuko zomwe boma lake lakwaniritsa monga  kuchepetsa chiwerengero cha nduna za boma komanso  kumanga sukulu zophunzitsa ntchito zamanja zam'madela.

Mayi Banda ndi Okhudzidwa ndi Imfa ya a Nyondo

$
0
0

Pamene atsogoleri osiyanasiyana pandale akupitiliza kusonyeza kukhudzidwa kwawo ndi imfa ya mtsogoleri  wachipani cha National Salvation Front NASAF a James Nyondo, mtsogoleri wakale wa dziko lino mayi Joyce Banda ati dziko lino lataya munthu ofunikira kwambiri.

A James Nyondo amwalira lachisanu kuchipatala cha Steve Biko Academic mdziko la South Africa atadwala matenda a khansa ya mmapapu.

Chikalata chomwe akuofesi ya mtsogoleri wakaleyu atulutsa lamulungu chati malemu Nyondo anali munthu wa masomphenya aakulu pa zatsogolo la dziko lino, ndipo asadamwalire wakhala akukambirana naye nkhani zosiyanasiyana zokhudza chitukuko.

Padakali pano akubanja la Nyondo akukonza zobweretsa thupi la malemuwa mdziko muno.

A James Nyondo adayamba kupikisana nawo pa mpando wa pulezidenti ngati mtsogoleri oyima payekha mchaka cha 2009, ndipo adayimanso paudindowu pachisankho cha pa 20 May 2014.

Anthu 15 Afa ndipo 10 Avulala Atawomberedwa

$
0
0

Anthu khumi ndi asanu aphedwa ndinso ena khumi avulala atawomberedwa ndi anthu ena omwe anakwera ngamila mdziko la Sudan.

Mmodzi mwa anthu omwe avulala pachiwembucho wawuza atolankhani kuchipatala komwe amugoneka,kuti anthu omwe achita chiwembucho amachokera kokawona abale awo mdera lomwelo, ndipo achita izi pomwe amabwerera kwawo lachiwiri sabata ino.

Anthu a mdera  lakuzambwe kwa dzikolo komwe chiwembucho chachitikira, ati amakhala mosatsata  malamulo pochita zinthu zawo, kuyambira mchaka cha 2003 pamene mitundu ina ya anthu idayamba kuwukira boma lomwe limatsata kwambiri malamulo a mmayiko a chiluya, lomwe akuti limawasala kwambiri.

Anthu 300 sauzande ndi omwe aphedwa pakusamvanako,ndipo ena oposa 2 miliyoni anathawa mnyumba zawo.

Mitundu yambiri mdzikolo akuti imakanganira zinthu zofunika kwambiri pamoyo watsiku ndi tsiku kuphatikizapo madzi omwe mmadera ambiri amasowa chifukwa cha chipululu.

 

 

 

Nthambi za Chitetezo Zidzudzula za Imfa ya Msilikali

$
0
0

Nthambi za chitetezo mdziko muno za Polisi ndi Army zadzudzula imfa ya msilikali wa Army yemwe anaphedwa ndi apolisi loweruka pa 22 November nthawi ya 11 koloko usiku mumzinda wa Zomba.

Akuluakulu ochokera munthambi ziwirizi adzudzula za imfayi pamsonkhano wa atolankhani omwe anachititsa lachinayi mu mzinda wa Lilongwe.

Akuluakuluwo adzudzula apolisi atatu omwe akukhudzidwa ndi imfa ya msilikaliyo,amene padakali pano ali mmanja mwa apolisi, ndipo alangiza asilikali munthambi ziwirizi kuti adzikhala ndi khalidwe pa ntchito yawo.

Polankhulapo nduna yowona za Chitetezo mdziko muno Paul Chibingu wati apolisi ntchito yawo ndi kupereka chitetezo kwa nzika za dziko lino ndipo kuti akamagwira ntchito yawo ayenera kutsata malamulo.

Iwo atsindika kuti akuluakulu a Army ndi Police mdziko muno akugwilira ntchito limodzi pofufuza za nkhaniyi kuti apeze chowona chenicheni.

Mkulu wa polisi a Paul Kanyama mogwirizana ndi mkulu wachiwiri  wa Army a Ignancio Maulana mdziko muno atsimikizira a Malawi kuti dziko lino lipitilira kukhala la bata ndi mtendere, ndipo ati mchitidwewu usagawanikitse dziko lino.

 

 

Papa Frascisco Asayina Mgwirizano Woteteza Chilengedwe ndi Kuthetsa Mchitidwe Wozembetsa Anthu

$
0
0

M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francis wasayinirana mgwirizano ndi akuluakulu a m’mizinda ochokera mmaiko osiyanasiyana wofuna kuteteza chilengedwe komanso kuthetsa mchitidwe wozembetsa anthu.

 

Papa Francisco, wasayinirana mgwirizanowu ndi akuluakuluwa pa msonkhano wa masiku awiri okambirana mfundo ziwirizi, omwe likulu lampingowu linawakonzera kuyambira lachiwiri sabatalatha.

 

Potsimikiza za kufunika kwa msonkhanowu,mtsogoleri wampingo wakatolikayu wati kalata yokamba zakusintha kwa nyengo yomwe watulutsa, sikukamba zakusintha kwa nyengo kokha, koma zamavuto omwe anthu akukumana nawo pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku,kaamba koti ati sikotheka kusiyanitsa nkhani za chilengedwe ndi umoyo wa anthu.

 

Ku msonkhanowu komwe kunafika nthumwi makumi asanu ndi awiri 70,nthumwizo zagwirizana njira zosiyanasiyana zothanira ndi mfundo ziwirizi,ndipo mwapadera, akuluakulu a mmizindawa kapena kuti mameya pachingerezi,alonjeza kuti adzipereka kwathunthu polimbana ndi mavuto awiriwa. 

Banki Yaikulu pa Dziko lonse Ithandiza Dziko la Nigeria

$
0
0

Banki yaikulu pa dziko lonse ya  World Bank,  yalonjeza kuti ipereka ngongole ya  ndalama zokwana 2.1 biliyoni za America zothandiza kukonzera madera ena omwe gulu la zauchifwamba la Boko Haram lidawonga.

 

Malipoti a wailesi ya BBC ati   mtsogoleri wadzikolo Muhhamudu Buhari, wapempha bankiyi kuti itumize nthumwi zake mdzikolo kuti zikawonerere momwe ndalamazo zingagwilire ntchito.

Iye wati ndalamazo, mwazina, zigwiritsidwa ntchito yomangira nyumba zomwe zigawengazo zidawononga, komanso kuthandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi zamtopola zomwe gululo lakhala likuwononga.

Pulezidenti wa dziko la America Barack Obama,  walonjezanso kuti athandiza dziko lake  ndi ndalama zokwana 5 miliyoni dolazi za America zolimbanira ndi gululo , potsatira chidwi chomwe pulezidenti Buhari wawonetsa pofuna kuthana ndi mchitidwe wauchifwamba mdzikolo.

Padakali pano pulezidenti Buhari walonjeza kuti achita chotheka kukambirana ndi akuluakulu a gulu la zigawengalo, pofuna kuti amasule asungwana oposa mazana awiri omwe akuwasunga mokakamiza kuyambira chaka chatha.


Anthu 40 Afa pa Nyanja ya Mediterranean

$
0
0

Anthu pafupifupi makumi anayi amila mu nyanja ya Mediterranean mdera lina lomwe lili kufupi ndi dziko la Libya bwato lomwe anakwera litamila.

Panthawiyi anthuwo ati anali paulendo opita mmayiko akuulaya pothawa umphawi mmayiko awo.

Anthu makumi asanu ndi anayi mwa anthuwo ati apulumutsidwa, ndipo padakali pano afika mdziko la Italy.

Bungwe la mgwirizano wa mayiko padziko lonse la United Nations lati anthu oposa zikwi makumi asanu ndi imodzi 60 sauzande ndi omwe apezeka akuthawa mmayiko awo kamba ka umphawi chaka chino chokha kuchokera kunsi kwa chipululu cha Sahara.

Dayosizi ya Mangochi Ichita Chikondwelero cha Nkhoswe Yake

$
0
0

Ntchito yokonzekera mwambo wokondwelera nkhoswe ya Dayosizi ya Mangochi yomwe ndi Augustino woyera ikupitilira.

Polankhula ndi Radio Maria Malawi mkulu woona zautumiki mu dayosiziyi Bambo Raphael Nkuzi ati episkopi wa dayosiziyi ambuye Montifort Stima achiwona chofunikira kwambiri kuti mwambowu ukachitikire m’boma la Balaka pofuna kuthandiza akhristu a m’bomali kuti asadzayende mtunda wautali.

Pamwambowu pakuyembekeza kudzakhala zochitika zosiyanasiyana kuphatikizapo kutolera thandizo la ndalama zomwe zidzathandize kuyendetsa Dayosiziyi.

Pulezidenti Obama Ayendera Dziko la Kwawo

$
0
0

Mtsogoleri wadziko la America Barrack Obama wafika  mdziko la Kenya paulendo wake ocheza mdzikolo, pomwenso akuyembekezeka kukambirana ndi atsogoleri a dzikolo pa nkhani zosiyanasiyana.

Paulendowu  ayamba wayima kulikulu la bungwe la mgwirizano wa amayiko a mu Africa la African Union AU ku Addis Abbaba mdziko la Ethiopia.

Aka kakhala koyamba kuti pulezidenti Obama afike mdziko la Kenya  komwe bambo ake anabadwira chitengere udindo wa pulezidenti mdziko la America.

Pulezidenti Obama akuyembekezeka kukambapo pankhani zokhudza chitetezo cha mmayiko a muno mu Africa, za malonda komanso nkhani zokhudza ndale,umphawi ndi maufulu a anthu.

Paulendowu,pulezidenti Obama ali ndi mlangizi pankhani ya chitetezo mdziko la America Susan Rice ndi akuluakulu ena.

A ku Banja Adzudzula Madonna Polephera Kusunga Lonjezo

$
0
0

Katswiri woyimba nyimbo za chamba cha POP wa mdziko la America Madonna, amudzudzula kamba kolephera kusunga lonjezo lomwe anapereka kwa makolo a mwana yemwe anamutenga mdziko muno kuti akamulere mdziko la kwawo.

Mayi Lucy Chekejiwa omwe ndi gogo wa Mercy James mmodzi mwa ana omwe iye adawatenga ndi omwe anena izi pofotokozera Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre.

Gogo Chekejiwa ati zaka zisanu ndi ziwiri zadutsa kuchokera pomwe Madonna anatenga mwanayo  koma mpaka pano, aku banja sadamuonepo.

Iwo ati ndi zodandaulitsa kuti Madonna amafika mdziko muno koma safuna kuwadziwitsa a ku banja  kuti mwanayo wafika mdziko muno.

“Ndakhala ndikudikira kuti mwina mwana abwera ndidzacheze naye, koma chimutengere sanayambe wabwerapo, mwanayo ndi wathu tikufuna titamuona,” anatero mayi Chekejiwa.

Iwo ati achita izi kamba kopwetekedwa mtima poganizira nthawi yomwe yadutsa asadamuone mdzukulu wawo ndipo apempha onse omwe angathe kuti alowelerepo pofuna kupeza mwayi womuona mwana wawo.

Madonna anatenga ana awiri a masiye mdziko muno David Banda ndi Mercy James kuti akawalere mdziko lakwawo ndipo pulezidenti wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika sabata yatha wasankha katswiri woyimbayu kuti akhale kazembe pa kasamalidwe ka ana.

 

Buhari Akumana ndi Pulezidenti wa Dziko la Cameroon

$
0
0

Mtsogoleri wa dziko la Nigeria Muhammadu Buhari lachitatu akuyembekezeka kukakumana ndi mtsogoleri wa dziko la Cameroon a Paul Biya kuti akakambirane mfundo zofuna kuthetsa gulu la zauchifwamba la Boko Haram.

Malipoti a News 24 ati chimukhazikitsire pa udindowu Pulezidentiyu wayenderapo kale mayiko a Chad ndi Niger omwe ndi oyandikana ndi dzikoli pofuna kupeza njira zothanira ndi gululi.

Anthu zikwizikwi mmayikowa akhala akuchitiridwa ziwembu ndi gululi kamba kofuna kukhazikitsa ulamuliro wa chisilamu mdziko la Nigeria.

Viewing all 1875 articles
Browse latest View live


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>