Mpingo wakatolika mdziko muno lachiwiri ukhazikitsa kalata yomwe mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco, walemba pankhani yokhudza chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo la Laudato Si.
Polankhula ndi Radio Maria Malawi, mlembi wamkulu wabungwe la maepiskopi mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM) Bambo Henry Saindi ati maepisikopi mdziko muno aganiza zokhazikitsa kalatayi mdziko muno poyang’anira mfundo zomwe zili mkalatayi zomwenso zikukhudza kwambiri dziko lino.
Iwo ati kalata yomwe Papa Francisco walemba ndi pempho lalikulu kwa anthu padziko lonse lapansi kuti akhale ndi udindo osamalira zachilengedwe potengera momwe kuwonongeka kwa chilengedwe kukukhudzira anthu.
“ifeyo ngati mpingo kuno ku Malawi takoza mwambo woti kalata ya Apapa francisco ya Laudato si yonkhuzana ndikusintha kwa nyengo ikhazikitsidwe kuno ku Malawi ”
Iwo anati chimene chapangisa kuti pabwele ganizoloti ankhazikitse kalata ya Apapa ndi chifukwa choti Malawi wankhuzidwa ndikusintha kwa nyengo mzaka zimenezi.
“ife tikuwona kuti kalata ya Apapa yonkhuza chilengedwe ndimwayi chifukwa choti ikupereka mayankho kumavuto womwe dziko la Malawi lankhala likukumana nawo, anthu ambiri nyumba zawo zinangwa chifukwa chama floods amene analipo, minda, mbewu zomwe adabyala zinakokoloka.” Bambo Henre Saindi anatelo
“Ma episcope anthu aganiza zonkhazikitsa kalata yomweyi ya apapa kuti unthenga womwe Apapa alemba mu kalata yayo owapatsa anthu udindo wosamalila chilengedwe m’dziko lomwe akunkhala ufike kwa wina aliyense” anawonjezera motelo Bambo Henry Saindi
Mwambo onkhazitsa kalatayi kuno ku Malawi uchitika ku Bingu International Conference Center M’dzinda wa Lilongwe.