Gulu lina la achinyamata lomwe langokhazikitsidwa kumene la JUBILLEE 50 MOVEMENT, lati atsogoleri omwe akhala akulamulira dziko lino alephera kukwaniritsa kukweza ntchito za chuma m'dziko muno.
Mamembala agululi ati ngakhale kuti dziko la Malawi likhale likukwanitsa zaka 50 lili pa ufulu odzilamulira posachedwapa, anthu akuyenera kuvomereza kuti atsogoleri omwe akhala akulamulira dziko lino, alephera kuthetsa mavuto azachuma omwe dziko lino lakhala likukomana nawo. Gululi lati izi zili chomwechi kaamba koti atsogoleri olamulira, akumangotanganidwa ndi ntchito za ndale osati zachitukuko monga momwe zimayenera kukhalira. Pamenepa mamembala aguliri ati ndi bwino kuti anthu adzasankhe atsogoleri a chinyamata, omwe mukuona kwawo akuti ndi omwe angathandize kukweza chuma cha dziko lino.