Bwalo la milandu la magistrate m'boma la Ntchisi lalamula mwamuna wina wa zaka 27, kuti akakhale kundende zaka zisanu ndi zitatu (8), atapezeka olakwa pa mlandu woba fetereza ndi mbewu za ndalama zoposa MK 4.9 million ku kampani ya Export Trading .
Mneneri wa apolisi m'bomalo Seargent Gladson M’bumpha wati mwamunayo Steven Kalipinde, anaba matumba a feteleza wa Urea okwana 202 komanso wa NPK ku kampaniyo. Wapolisi otengera milandu kubwalo la milandu , Constable Austin Daudi, anauza bwalolo kuti a Kalipinde, anabanso mbeu ndi katundu wina zomwe ndi zandalama zoposa 4.9 million kwacha. Popereka chigamulo chake magistrate Dorothy Kalua, anati wapereka chilango chokhwimacho kuti anthu ena atengerepo phunziro. A Steven Kalipinde amachokera m'mudzi wa Chipho kwa mfumu yaikulu Msabwe mboma la Thyolo.