Mpingo wa CHURCHES OF CHRIST m’boma la MANGOCHI wati ukudzipeleka kwambiri pogwira ntchito za chifundo pambalinso pogwira ntchito zofalitsa uthenga wa chipulumutso,
M`busa Denson Mulaleya wa mpingowu m'boma la MANGOCHI ndi yemwe walankhula izi ndi mtolankhani wathu, yemwe amafuna kudziwa zolinga za maphunziro omwe mpingowu unali nawo kudera la NAVEYA mboma la BALAKA. A MULALEYA ati mpingo wawo umadziwa zakufunika kotengapo mbali pogwira ntchito za chifundo, moti posachedwapa , amayi a mpingowu akhala akukacheza ndi odwala pa chipatala chachikulu m`boma la MANGOCHI.