Chipani chotsutsa boma cha umodzi chalangiza m’tsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharikakuti asavomereze Bilo yatsopano yokhudza malo yomwe nyumba ya malamulo yakhala ikukambirana.
M’tsogoleri wa chipanichi Professor John Chisi walankhula izi ndi atolankhani mu mzinda wa Blantyre.
Professor Chisi wati bilo yatsopano-yi ndiyosathandiza a Malawi kaamba koti ikupereka mphamvu kwa nduna kuyang’anira nkhani za malo m’dziko muno zomwe zikusonyeza kuti ikavomelezedwa ndiye kuti ndi mafumu sadzidzakhala ndi mphamvu pa nkhani zokhudza malo.
“Bilu imeneyi siyopindulira a Malawi. Bilu imeneyi ikufuna kuchotsa mphamvu kwa anthu ndi kuzipereka kwa nduna. Ndunayi ndimene izakhale ndi mphamvu zogula malo paliponse, mafumu sazakhala ndi mphamvu iliyonse. Akuziwa kumene kuli miyala ya mtengo wapatali ili ndiye akufuna agule malo ngati amenewo agulitse kwa anzawo ma China ndi cholinga choti akadzachoka pa mpando asadzasowe pogwira. Sakufuna kuti PAC ikambirane, bilu ya access to information sakufuna kuyivomereza. Akufuna azitibera mpaka muyaya. Ife takana,” anatero Professor Chisi.
Iwo anapempha president kuti ngakhale aphungu adutsitse biluyi iye asasayinire biluyi kukhala lamulo.
“A presidenti amanena kuti patriotism and integrity ndiye ngati ali ndi integrity asasayinire biluyi. Ngati akuti patriotism sangalore kuti mbadwo umene ukubwerawu usazadyelere. Kayerekera watikanika ndiye akufuna kuti anthu amene akulongolorawo asazakhalenso ndi mawu. Anzathu a dpp tikondeni kondani dziko lathu. Tinakupatsani mwayi kuti mutilamulire. Ma bilu ngati amenewa akusonyezeratu kuti mulibe chikondi kwa ife. Mutikonde koyenera ndipo muzipanga zinthu zokomera a Malawi tonse,” anatero Professor Chisi.