Sukulu ya m’mera mpoyamba ya St. John m’boma la Mangochi yati ipitiriza kudzipeleka pa ntchito zokweza maphunziro a ana a m’dera la Senior Chief Chimwala ndi madera ena m’boma la Mangochi.
A Martin Milanzi omwe anayimira mkulu wa sukuluyi bambo Joseph Kimu ndi amene anena izi pakutha pa mpikisano wa zamaphunziro umene anachititsa kwa ana amene anaphunzirapo pa sukulu-yi ndi ya Bishop Assolari kwa Kausiyomwe ikupezeka m’dera la mfumu yayikuluyi.
A Milanziati sukulu-yi inaganiza zokonza mpikitsano-wu ngati njira imodzi yothandiza pa ntchito zokweza maphunziro a wana m’delaro.
Ana omwe anachita nawo mpikisano-wu ndi omwe achita bwino pa mayeso awo otsiriza a chaka chino ndipo anali okhawo omwe akhala nambala one mpaka nambala 10. Anawa anali ochokera msukulu za primary za Chimwala, St.John, Kausi, Likala ndi Changamire.
Malingana ndi dongosolo la mpikisanowu ana omwe anapambana mayeso omwe anapatsidwa mu mpikitsano-wu kuyambira pa nambala 1mpaka nambala 3mu kalasi ina ili yonse analandira mphatso zosiyanasiyana monga makope, zikwama, zolembera ndi zipangizo zina zophunzilira .