Achinyamata mu mpingo wakatolika awapempha kuti adzipereke polowa m’mautumiki osiyanasiyana opezeka mu mpingowu.
Bambo Medrick Chimbwanya anena izi ku Parish ya Ulongwe m’boma la Balaka pomwe amachita chaka chokondwelera kuti akwanitsa zaka 25 akutumikira Mulungu ngati wa msembe mu mpingo wa katolika mu dayosizi ya Mangochi.
Iwo ati chimodzi mwa zinthu zomwe akufuna kuzikwanitsa mu zaka zikubwerazi ndi kulimbikitsa achinyamata kuti adzipereke potumikira Mulungu kudzera mu njira ya unsembe ndi m’mautumiki ena mu mpingo-wu, zomwe ati zithandiza kuti mpingo-wu upitilire kukhala ndi atumiki ochuluka.
“Ndine wokondwa kwambiri kuti ndakwanitsa zaka zimenezi mu unsembe koma ndikudziwa kuti siine wopambana, Mulungu ndiye amene wandikomera mtima pondisankha kukhala wansembe komanso mphatso zina zomwe anandipatsa kuti ndimutumikire.
Ndipemphe achinyamata kuti tikamamva uthenga kutchalitchi uzitikhudza. Pali zosangalatsa zambiri inde koma ndi zakutha ndi zotsala pamene ufumu wa Mulungu suzatha konse. Tipitirize mphatso imene Mulungu anatipatsa ngati akhristu potumikira anthu ambiri pa dziko la pansi amene akusowa chipulumutso,” anatero bambo Chimbwanya.
Mlendo wolemekezeka pa mwambowu anali a episikopi a dayosizi-yi olemekezeka ambuye Montfort Stima.
M’mawu awo ambuye Stima, afunira zabwino bamboo Chimbwanya kamba kodzipereka potumikira mulungu kwa zaka zochulukazi ngati wansembe wa mpingo wakatolika mudayosizi-yi.
Bambo Medrick Chimbwana anadzodzedwa umsembe ndi malemu ambuye Allesandro Asolarimchaka 1991.