Dziko la Morocco latumiza thumwi kuti zikambirane ndi atsogoleri a abungwe la mgwirizano wa maiko a mu Africa la African Union(AU) kuti dzikolo lilowenso m`gulu la AU patatha 32 dzikola Morocco litatuluka mubungweri.
Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC, dzikori linatuluka mubungweri kaamba koti bungwe la AU limatsutsa ganizo la dziko la Morrocoloti dera la kunzambwe kwa Sahara ndi mbali ina ya dzikolo.
Nthumwi za dzikolo zinakumana ndi mtsogoleri wa dziko la Kenya a Uhuru Kenyata ndipo anawauza kuti dzikolo lifufuna kulowanso m`bungwelo popanda mfundo komanso ndondomeko zilizonse.
Dziko la Moroccolimati dera la kuzambwe kwa Sahara ndi mbali ya dziko lake pomwe bungwe la AU limatenga derali ngati dziko loima palokha.
Morocco ndi dziko limodzi lokha lomwe silili mu bungwe la AU pa maiko onse amuno mu Africa.