M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisko wati ndi wokhudzidwa ndi imfa ya anthu 80 omwe anaphedwa pa chiwembu china chomwe chachitikanso m’dziko la France sabata ikongothayi.
Pa chiwembuchi munthu wina amene amayendetsa galimoto la mtundu a Track anakaomba anthu amene anasonkhana malo ena kuwonelera masewera ena omwe amachitika m’dzikomo, ndipo anapha anthu oposera 80 ndi kuvulaza ena ambiri pa malopo.
Chiwembuchi chinachitika potsatira chiwembu china chomwe chinachitika m’dzikomo miyezi yapitayi.