Aphunzitsi achikatolika mu dayosizi ya Dedza awapempha kuti akhale olimbika ndi okhulupilika pa ntchito yawo.
Mlembi wa za maphunziro msukulu za chitolika mu dayosizi-yo a Zakaliya Pengapenga ndi omwe anena izi pomwe amachita zokambilana ndi aphunzitsi-wa mu dayosiziyo. Msonkhano-wu unachitikira pa sukulu ya mpingo-wu ya Dedza, loweluka pa 16 July 2016.
Iwo ati aphunzitsi-wa akuyenera kumadzipeleka pa ntchito yawo ndi kuti ana ambiri msukuluzi azichita bwino pa zotsatiura za mayeso awo.