Pomwe aphungu akunyumba ya malamulo avomereza bilo yokhudza malo lachinayi pa 13 July 2016, Anthu ena ati sakugwirizana ndi biloyi ponena kuti ithetsa ufumu chifukwa popanda malo ntchito ya ufumu pakhala palibe.
Iwo ati biloyi siyopindulira kwenikweni amalawi kaamba koti ikupereka mphamvu kwa nduna ya zamalo kuti ikhoza kugulitsa malo nthawi inailiyonse.
Mfundo yomwe yakwiyitsa mafumu ambiri ndi yoti malo a makolo omwe ali m’manja mwa mafumu azikhala mmanja mwa anthu.
Mafumu ena a m’maboma a Mzimba, Chikwawa komanso Lilongwe ati malo ambiri amatetezedwa ndi mafumu ndipo anthu amawopa kugulitsa malo popanda mfumu kudziwa. Mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) Dr. Lazarus Chakwera wagwirizana ndi mafumu wa ponena kuti biluyi ndi yosawukitsa a Malawi.
Nduna ya za malo ndi chitukuko cha m’madera wolemekezeka Atupele Muluzi ati kwakula ndi kusamvetsetsa kwa anthu pa biluyi.
Mwa aphungu 124 amene anaponya mavoti, 65 anavomera kuti biluyi idutse.
Izi zadza patangopita tsiku limodzi aphungu ena otsutsa atatuluka mnyumbayi kamba kosagwirizana ndi magawo ena a biluyi.