Bungwe la mgwirizano wa maiko pa dziko lonse la United Nations (UN) ladzudzula gulu la zauchifwamba la Boko Haram kaamba ka zamtopola zomwe likuchitira anthu a m’dziko la Nigeria.
M’modzi mwa akuluakulu a bungweli, a Stephen O’brienati zomwe guluri likuchita zachititsa kuti anthu zikwizikwi athawe mdzikoli ndi kusiya ena akusowa thandizo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC anthu oposa 9 million akusowa thandizo mdzikolo kutsatira ziwembu zomwe gululi lakhala likuchita.
Malinga ndi malipoti kuchokera mwezi wa January chaka chino kufikira mmwezi wa June ana oposa 50 ndi amene akakamizidwa kuvala ma bomba a tikenawo m’maiko anayi ozungulira dzikolo.