Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Fransisko Wapempha Dziko la Poland Lizilandira Anthu Othawa Kwawo

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha atsogoleri a zipani mdziko la Poland kuti azilandira anthu othawa kwao ochokera m’maiko osiyanasiyana.

Papa amalankhula izi mdzikolo pa mkumano omwe anali nawo ndi mtsogoleri wa dzikolo, nduna yaikulu ya dzikolo komanso atsogoleri a zipani zosiyanasiyana za mdzikolo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa wati potsatira mavuto omwe maiko akukumana nawo kuphatikizapo nkhani za chuma, anthu akuyenera kukhala okonzeka kulandira anthuwa omwe akuthawa mmaiko awo kaamba ka nkhondo, kusowa kwa ntchito ngakhalenso kuphwanyiridwa ma ufulu awo.

Pamenepa Iye wati pakuyenera kukhala mgwirizano wabwino pofuna kuthetsa mavuto omwe akuchititsa kuti anthuwa azithawa mmaiko awo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>