Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Catholic Charasmatic Renewal Movement Ikondwelera Zaka 25

$
0
0

Mwambo wa msembe ya misa wokondwelera kuti bungwe la Catholic Charasmatic Renewal Movement (CCRM) lampingo wakatolika lakwanitsa zaka 25 chilikhazikitsileni m’dziko muno wachitika ku Maula Cathedral mu arkdayosizi ya Lilongwe.

Poyankhula pa mwambowu Arkiepiskopi wa arkidayosizi ya Lilongwe, Ambuye Tasizio Ziyaye, omwe anatsogolera mwambowu ati akhristu akuyenera kusaukira chikhulupiliro pomwe makono ano chikhulupiliro chathu chikuyesedwa ndi maphunzitso omwe sakugwilizana ndi chikhristu.

“Mdziko lapansi mukubwera maphunziro onama osagwirizana ndi chikhristu ndipo satana amanyengelera anthu. koma ife tizikhulupilira mulungu amene ali wosamana ndi wosanyengeza komanso kulimba mtima kusawukira chikhulupiliro chathu ngakhale ena atinyoze,” anatero Ambuye Ziyaye.

Pa mwambowu panafika alendo ochokera m’maiko a Italy, United Kingdom komanso anthu ena ochokera mmadayosizi a mpingowu mdziko muno.

Bungwe la Catholic Charasmatic Renewal Movement linayamba mchaka cha 1967 ndi ophunzira a pa sukulu ya ukachenjede ya Tukkein mdziko la america. kuno ku Malawi bungweli linayamba mchaka cha 1991 ku Maula Cathedral mu arkidayosizi ya Lilongwe.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>