Polankhula moyimira achinyamata-wa bambo Frank Mwinganyama omwe ndi mlangizi wa achinyamata mu Arch-Dayosizi ya Blantyre omwenso anali nawo pa ulendowu ati ndi okhutira ndi momwe chakachi chayendera. “Anatilandira bwino ku dayosizi ya Opole komwe tinatenga nawo mbali pa zisangalaro zosiyanasiyana ndipo tinagwira nawo ntchito zachifundo komanso kupemphera ku malo oyera a kumeneko” Anatero Bambo Mwinganyama.
“Tinali ndi mwayi ocheza ndi anzathu kuwauza zambiri za dziko lathu la Malawi, ndipo zinali zodabwitsa kumva kuti ena samadziwa kuti dziko la Malawi lilipo padziko pano koma titawauza zambiri zokhudza malo athu opatsa chidwi a zokopa alendo anamvetsa ndipo alonjeza kuti adzabwera pa nthawi yawo ya tchuti mtsogolo muno” Anawonjezera bambooMwinganyama.
Achinyamata okwana khumi ndi asanu ndiomwe anakaimilira mpingo wakatolika ku nsonkhanowu chaka chino.