Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Kabwira Akufunitsitsa Apolisi Afufuze Mokwanira za Kuwotchedwa kwa Galimoto Lake

$
0
0

Phungu wa kunyumba yamalamulo m’chingawo chakumpoto cha kumvuma kwa boma la Salima, olemekekezeka Dr. Jessie Kabwira  wati akufunitsitsa kuti  apolisi afufuze mokwanira nkhani ya kuotchedwa kwa galimoto yawo posachedwapa ku Golf Club mu mzinda wa Lilongwe.

Dr. Kabwila anena izi ku Chitala m`bomali pamsonkhano wachitukuko  ndipo ati anthu a m`derali asade nkhawa pa zakuontchedwa kwa galimoto lawo zomwe iwo ati awonetsetsa kuti apolisi afufuze mwaukadaulo.

Akabwira anati akuganiza kuti chipongwechi anachita ndi anthu achipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP). Iwo anati posachedwapa nduna yofalitsa nkhani omwe ndi mayi Patricia Kaliati, inalengeza kuti aKabwira athana nawo kamba koti akhala akudzudzula boma kuti lithane ndi mavuto omwe dziko lino likukumana nawo.

Mwazina, phunguyu anatsimikizila anthu zamgwilizano omwe bungwe la Christian Health Association of Malawi (CHAM) linasainirana ndi boma loti amayi oyembekezera  mderali sazilipira akafuna kukachira kuzipatala za CHAM.

Galimoto la aKabwira linaotchedwa posachedwapa ku Lilongwe Golf Club pomwe iwo anali pa nkumano ndipo pakadalipano apolisi akufufuza kuti apeze anthu omwe akukhudzidwa pankhani-yi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>