Kuyenderana pakati pa achinyamata a m`bungwe la Young Christian Workers (YCW) ati kungathandize kuti ntchito za bungweri zipite patsogolo.
Wapampando wa bungwe la YCW ku St. Charles Luangwa m`dayosizi ya Zomba, Peter Kafwafwa Banda ndiye wanena izi pomwe achinyamata abungweri anakayendera achinyamata anazawo ku St. Pius Parish mu arkidayosizi ya Blantyre.
Iye wati pomwe achinyamatawa akhala pamodzi amakambirana zambiri zokhudza bungwe lawo komanso moyo wawo ndikulimbikitsana patchito zachifundo zomwe bungweri limachita. Kafwafwa Banda akufotokoza.
“Zimalimbikitsa ubale wathu ngati YCW komanso matchalitchi awiri akuyenderanawo. Zimatithandizanso kulimbitsa moyo wathu wa uzimu ndi wa ku thupi. Tizikumanakumana kuti tizikambirana zotukula bungwe lathu,” anatero Banda.
Ndipo m`mawu ake wapampando wa bungweri ku St. Pius, Patrick Saizi anati nkumanowu wawanthandiza kuti akambirane za mavuto omwe achinyamatawa akukumana nawo.
“Mikumano imeneyi imathandiza kukambirana mavuto athu omwe timakumana nawo monga kusowa kwa ntchito komanso mavuto ena amene amaphinja umoyo wathu. Timapeza mfundo zomwe zingachepetse mavutowa. Timakambirananso za umoyo wathu wa uzimu,” anatero Saizi.
Bungweli lapempha achinyamata onse a mpingowu mdziko muno kuti akonde kulowa m’magulu osiyanasiyana mu mpingowu.