Mzika ina ya dziko la Democratic Republic of Congo (DRC), yafa itamwa mowa osadyera kumalo osungirako anthu othawa kwawo a Dzaleka m`boma la Dowa.
Wofalitsa nkhani za apolisi m`boma la DowaSergent Richard Kaponda watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati mamunayu ndi Kimongo Kalambo wazaka 37 zakubadwa ndipo amakhala yekha kunyumba kwake pamsasawu.
Malinga ndi abale ake, mkuluyu anachoka ndikupita kumalo ena omwera mowa komwe anakhalako masiku atatu akumwa opanda kudya chakudya.
Mneneri wa apolisiyu wali lipoti lakuchipatala lasonyeza kuti mkuluyu wafa kaamba komwa mowa osadyera. Mkuluyu amachokera m`dera la South Kivu m`dziko la DRC.