Apolisi munzinda wa Lilongwe amanga mwamuna wina wazaka 27 atampeza ndi minyanga ya njovu.
Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi munzindawu, Inspector Kingsley Dandaula, mkuluyi Ackim Bwanali amasunga minyangayi m`galimoto lake pamalo otsukira magalimoto ku Falls Estate munzindawu.
Ndipo apolisi mogwirizana ndi ogwira ntchito kumalo osungirako nyama zachilengedwe anafika pamalowa ndikupeza minyangayi m`galimotolo.
Mamunayu amachokera m`mudzi mwa Talirani kwa mfumu yaikulu Chowe m`boma la Mangochi. Apolisi apempha anthu m`dziko muno kuti adzikanena kupolisi ngati akudziwa kuti pali anthu ena omwe ali ndi minyanga yanjovu.