Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Chiwerengero cha Milandu Chakwera ndi 9.2% ku Chigawo cha Kum’mawa kwa Dziko Lino

$
0
0

Apolisi ku m’chigawo cha kum’mawa kwa dziko lino ati chaka chino chiwerengero cha milandu chakwera kwambiri m’miyezi isanu ndi umodzi (6) yapitayi poyerekeza ndi momwe zinaliri m’miyeziyi chaka chatha.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’chigawo cha kum’mawa kwa dziko lino, Inspector  joseph Sauka ndi yemwe wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.  A Sauka wati chiwerengerochi chakwera ndi 9.2 percent.

“Chaka chatha cha 2015 tinali ndi milandu yokwana 3658 pamene chaka chino cha 2016 tachita register milandu yokwana 3993 zimene zikuwonetsa kuti pali kusiyana kwa milandu 335 imene ikuyimira 9.2 percent,” anatero Inspector Sauka.

Iwo ati chiwerengero cha milanduchi chakwera motere kamba ka milandu ing’onoing’ono yomwe ingathe kupeweka ngati anthu alolerana pamene asemphana maganizo.

“Yachuluka ndi milandu ing’onoing’ono monga kumenyana. Zimenezi zikuchitika chifukwa anthu sakutha kumvetsetsana pamene alakwirana. Anthu akuyenera kumakhala pansi ndi kukambirana pamene asemphana Chichewa,” anatero Inspector Sauka.

Iwo ati apolisi m’chigawochi achita bwino pochepetsa milandu ikuluikulu imene imapereka chiwopsezo kwambiri kwa anthu monga monga kuthyola nyumba, kuba moopseza ndi mufti komanso kuphana.

Inspector Sauka athokoza anthu amene amatsina khutu apolisiwa kuti agwire ntchito zawo bwino komanso ayamikira magulu achitetezo akumidzi kamba koti ati akugwira ntchito yotamandika popereka chitetezo m’madera awo osiyanasiyana zomwe zikuchepetsa milandu ikuluikulu m’chigawochi.

Iwo apempha anthu mdziko muno makamaka m’chigawochi kuti aliyense atengepo gawo pochepetsa milandu m’madera awo komanso kuti akonde kukambirana pamene asemphana Chichewa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>