M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransiskowati ndi wokhudzidwa ndi mavuto akusowa kwa mtendere omwe anthu a m’dziko la Syria akupitilira kukumana nawo.
Papa wati magulu omwe akulimbikitsa nkhondo yapacheweniweni m’dzikomo, akuyenera kumvana chimodzi ndi kuthetsa kusagwilizana kwawo mwa msanga ndi kuti mtendere ubwelerenso m’chimake m’dzikomo.
M’tsogoleri wa mpingo wakatolika-yu wapereka uthenga-wo potsatira imfa ya anthu 13 omwe afa potsatira za mtopola zomwe gulu lina la zigawenga zowukira boma la dzikolo zachita ku kudera lina mdzikomo.
Mwa zina zigawengazi akuti zaononganso katundu wa pa chipatala china m’delaro.