Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Nyumba Zotsindika ndi Kuwulutsa Nkhani ati Zikuyenera Kuphunzitsa Chiphunzitso cha Mpingo

$
0
0

Nyumba zotsindika ndi kuwulutsa nkhani za mpingo wakatolika mdziko muno azipempha kuti nthawi zonse pamene zikugwira ntchito yake zizitsatira chiphunzitso chomwe mpingo wakatolika umaphunzitsa.

Episkopi wa dayosizi ya Zomba Ambuye George Desmond Tambala ndi omwe alankhula izi ngati mlendo olemekezeka lolemba ku Chipoka m’boma la Salima potsekulira maphunziro a sabata ziwiri omwe bungwe la maepiskopi a mpingo wa katolika la Episcopal Conference of Malawi ECM lakonzera akuluakulu ogwira ntchito mu nyumba zotsindika ndi kuwulutsa nkhani za mpingo wakatolika mdziko muno.

Iwo ati pozindikira kuti chiphunzitso cha mpingo ndi chomwe chimathandiza kutukula miyoyo ya akhristu, nyumbazi zikuyenera kuchilimika pa nkhaniyi.

“Ifeyo tisayiwale kuti ndife ndani tikuyenera kuti chuma chathu chomwe ndi chiphunzitso cha mpingo tikuchitsatira moyenera kamba koti miyoyo ya anthu ikutukuka,”anatero Ambuye Tambala.

Pamenepa Ambuye Tambala apempha nyumbazi kuti zizigwilira ntchito limodzi ngati ana a banja limodzi.

Ambuye Tambala anati,“sibwino kuti aliyense aziyenda payenkha, tikuyenera kugwira ntchito limodzi ngati ana a Eklezia kaamba koti tikatero titha kupanga zinthu za mtengo wapatali zopindulira mpingo wathu.”

Episkopiyu anapempha anthu omwe akuchita nawo maphunzirowa kuti nthawi zonse pamene akugwira ntchito yawo aziwonetsetsa kuti akulandira maganizo a anthu pa zomwe akuwapatsa.

Pomaliza Ambuye Tambala anati ali ndi chiyembekezo kuti maphunzirowa akhala othandiza kwa anthuwa kamba koti aphunzira njira zabwino zomwe zithandize kuti azigwira bwino ntchito yawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>