Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Wapepesa Dziko la Mexico, America

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Fransisko wapereka  uthenga wachipepeso kwa anthu omwe akhuzidwa ndi mphepo ya mphamvu yomwe yakhuza anthu a m’maiko a Mexico komanso America.

Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, anthu pafupifupi khumi ndi atatu (13) afa mdziko la America ndipo ena makumi anayi ndi asanu (45) afanso mdziko la Mexicopa ngoziyi.

Uthengawu waperekedwa kuzera ku bungwe la ma episkopi mdziko la Mexico la Mexican Episcopal Conference ndipo mu uthengawu Papa Fransisko wati  ndiokhuzidwa kamba ka ngoziyi ndipo wati ayikiza m’mapemphero onse omwe ataya miyoyo yawo ndi onse omwe avulala pa ngoziyi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>