Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Afa Atatsamwidwa ndi Chingamu

$
0
0

M`nyamata wina wa zaka zisanu ndi ziwiri (7) wafa atatsamwidwa ndi chingamu ku Bangwe munzinda wa Blantyre.

Malinga ndiwothandizira mu ofesi yazofalitsa nkhani pa polisi ya Limbe, Sergent Widson Mushani watsimikiza za nkhaniyi  ndipo wati malemuyi  wamwalira pa chipatala chaching`ono cha Namatapaasanalandire thandizo lamankhwala ndipo amachokera m`mudzi mwa  Mondiwa kwa mfumu yaikulu Machinjiri m`boma la Blantyre.

“M’nyamatayi pa 7 August anapita kukagula chingamu pa shop ina mderali. Akutafuna bubblegum anatsamwidwa ndi kukomoka. Anthu anamtengera ku Namatapa Health Centre komwe anamwalira akulandira chithandizo,” anatero Sergeant Mushani.

Iwo ati zotsatira za kuchipatala zatsimikiza kuti mwanayi wafa ndi chingamu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>