M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa Francisco wati ndi wokhudzidwa ndi imfa ya anthu anayi omwe afa kamba ka ngozi ya moto wachilengedwe umene unabuka mu nkhalango ina m’dziko la Portugal.
Motowo akuti unasakaza katundu wa ndalama zochuluka ndi nyumba za anthu okhala m’dela la Madeira lomwe lakutidwa ndi nkhalango yomwe inabuka motoyo.
Mwa anthu asanu omwe afa pa ngozi-yi m’modzi ndi wa m’dziko la Spain lomwe lachita malire ndi dzikolo.
Mu uthenga wake papa wati alimbikitsa mapemphero pakati pa mabanja omwe ataya achibale awo ndinso kwa omwe akhudzidwa pa ngoziyo.