Nthambi yoona za chitukuko mu mpingo wa katolika ya Catholic Development Committee (CADECOM) mu dayosizi ya Zomba yati atolankhani ali ndi udindo waukulu ophunzitsa anthu kuyipa kwa matenda akunyetchera mdziko muno.
Mkulu woona za umoyo munthambiyi mai Arsenia Kasonga Banda omwe analankhula izi ku Liwonde m’boma la Machinga pakutha pa maphunziro omwe anakonzera atolankhani anyumba zosiyanasiyana zoulutsira mau ndi kulemba nkhani komanso azitsuzo ndi cholinga chowapatsa ukadaulo wa m’mene angafufuzire ndikulembera nkhani ndicholinga chofuna kuthana ndi kunyetchera kwa ana.
“Poyamba ana amene akunyentchera anali pa 47 percent ndipo pakadali pano ndi chithandizo cha atolankhani, azisuzo komanso adindo mmidzi zikusonyeza kuti zikuyenda ndithu mpaka tafika pa 35 percent. ndiye tikupempha atolankhani ndi ena kuti atithandizebe kuti matendawa atheretu,” anatero Kasonya Banda.
M’modzi mwa atolankhani omwe anachita nawo maphunzirowa a Augustine Muotcha kuchokera ku wailesi ya YONECO anathokoza bungweli kamba ka chidwi chomwe lili nacho pachepetsa matenda akunyentchera mdziko muno ndipo analonjeza kutengapo gawo lalikulu polemba nkhani za mtunduwu kuti anthu ambiri azindikire kuyipa kwa matendawa.
“Tadziwa kuti matendawa ndi oopsa komanso taphunzira njira zimene tingawawfikire anthu akumidzi. ife ngati atolankhani tigwirana nawo manja pa ntchitoyi,” anatero a Muotcha.